1. Koma za nthawizo ndi nyengozo, abale, sikufunika kuti tidzakulemberani,
2. Pakuti inu nokha mudziwa bwino kuti tsiku la Ambuye lidzadza monga mbala usiku,
3. Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo cionongeko cobukapo cidzawagwera, monga zowawa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse.
4. Kama inu, abale, simuli mumdima, kuti tsikulo likakugwereni monga mbala;
5. pakuti inu nonse muli ana a kuunika, ndi ana a usana; sitiri a usiku, kapena a mdima;
6. cifukwa cace tsono tisagone monga otsalawo, komatu tidikire, ndipo tisaledzere,
7. Pakuti iwo akugona agona usiku; ndi iwo akuledzera aledzera usiku.