1 Atesalonika 2:13-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo mwa icinso ife tiyamika Mulungu kosalekeza, kuti, pakulandira mau a Uthenga wa Mulungu, simunawalandira monga mau a anthu, komatu monga momwe ali ndithu, mau a Mulungu, amenenso acita mwa inuokhulupirira.

14. Pakuti inu, abale, munayamba kukhala akutsanza a Mipingo ya Mulungu yokhala m'Yudeya mwa Kristu Yesu; popeza zomwezi mudazimva kowawa nelinunso pamanja pa a mtundu wanu wa inu nokha, monganso iwowapa manja a Ayuda;

15. amene adaphanso Ambuye Yesu, ndi aneneri, natilondalonda ife, ndipo sakondweretsa Mulungu, natsutsana nao anthu onse;

16. natiletsa ife kuti tisalankhule ndi akunja kuti apulumutsidwe; kudzaza macimo ao nthawi zonse; koma mkwiyo wafika pa iwo kufikira cimariziro.

1 Atesalonika 2