11. Pakuti mwa cidziwitso cako wofokayo atayika, ndiye mbale amene Kristu anamfera.
12. Koma pakucimwira abale, ndi kulasa cikumbu mtima cao cofoka, mucimwira kotero Kristu.
13. Cifukwa cace, ngati cakudya cikhumudwitsa mbale wanga, sindidzadya ayama ku nthawi yonse, kuti ndiogakhumudwitse mbale wanga.