8. Koma ndidzakhaia ku Efeso kufikira Penteskoste,
9. Pakuti panditsegukira pa khomo lalikuru ndi locititsa, ndipo oletsana nafe ndi ambiri.
10. Koma akadza Timoteo, penyani kuti akhale ndi inu wopanda mantha; pakuti agwira nchito ya Ambuye, monganso ine;
11. cifukwa cace munthu asampeputse, Koma mumperekeze mumtendere, kuti akadze: kwa ine; pakuti ndimuyembekezera pamodzi ndi abale,
12. Koma za Apolo, mbaleyo, ndamuumiriza iye, adze kwa inu pamodzi ndi abale; ndipo sicinali cifuniro cace kuti adze tsopano, koma adzafika pameneaona nthawi.
13. Dikirani, cirimikani m'cikhulupiriro; dzikhalitseni amuna, limbikani.
14. Zanu zonse zicitike m'cikondi.
15. Koma ndikupemphani inu, abale, (mudziwa banja la Stefana, kuti ali cipatsocoundukula ca Akaya, ndi kuti anadziika okha kutumikira oyera mtima),