1 Akorinto 16:14-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Zanu zonse zicitike m'cikondi.

15. Koma ndikupemphani inu, abale, (mudziwa banja la Stefana, kuti ali cipatsocoundukula ca Akaya, ndi kuti anadziika okha kutumikira oyera mtima),

16. kuti inunso mubvomere otere, ndi yense wakucita nao, ndi kugwiritsa nchito.

17. Koma ndikondwera pa kudza kwao kwa Stefana, ndi Fortunato, ndi Akayiko; cifukwa iwo anandikwaniritsa cotsalira canu.

1 Akorinto 16