35. Koma ngati afuna kuphunzirakanthu afunseamuna ao aiwo okha kwao; pakuti kunyazitsa mkazi kulankhula mu Mpingo.
36. Kodi mau a Mulungu anatutuka kwa iw? kapena anafika kwa inu nokha?
37. Ngatiwinaayesa kuti ali mneneri, kapena wauzimu; azindikire kuti zimene ndilemba kwa inu ziri lamulo la Ambuye,
38. Koma ngati wina akhale wosadziwa, akhale wosadziwa.
39. Cifukwa cace; abale anga, funitsitsani kunenera, ndipo musaletse kulankhula malilime.
40. Koma zonse zicitike koyenera ndi kolongosoka.