1 Akorinto 14:14-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Pakuti ngati ndipemphera m'lilime, mzimu wanga upemphera, koma cidziwitso canga cikhala cosabala kanthu.

15. Kuli ciani tsono? Ndidzapemphera ndi mzimu, koma ndidzapempheranso ndi cidziwitso canga; ndidzayimba ndi mzimu, koma ndidzayimbanso ndi cidziwitso.

16. Cifukwa ngati udalitsa ndi mzimu, nanga iye wakukhala wosaphunzira adzati Amen bwanji, pa kuyamika kwako, popeza sadziwa cimene unena?

17. Pakutitu iwe uyamika bwino, koma winayo samangiriridwa.

18. Ndiyanillca Mulungu kuti ndilankhula malilime koposa inu nonse;

19. koma mu Mpingo ndifuna kulankhula mau asanu ndi cidziwitso canga, kutinso ndikalangize ena, koposa kulankhula mau zikwi m'lilime.

20. Abale, musakhale ana m'cidziwitso, koma m'coipa khalani makanda, koma m'cidziwitso akulu misinkhu.

21. Kwalembedwa m'cilamulo, Ndi anthu amalilime ena ndipo ndi milomo yina ndidzalankhula nao anthu awa; ndipo kungakhale kutero sadzamva Ine, anena Ambuye.

22. Cotero malilime akhala ngati cizindikilo, si kwa iwo akukhulupira, koma kwa iwo osakhulupira; koma kunenera sikuli kwa iwo osakhulupira, koma kwa two amene akhulupira.

1 Akorinto 14