1 Akorinto 13:5-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. sicicita zosayenera, sicitsata za mwini yekha, sicipsa mtima, sicilingirira zoipa;

6. sicikondwera ndi cinyengo, koma cikondwera ndi coonadi;

7. cikwirira zinthu zonse, cfkhulupirira zinthu zonse, ciyembekeza zinthu zonse, cipirira zinthu zonse.

8. Cikondi sicitha nthawizonse, koma kapena zonenera zidzakhala cabe, kapena malilime adzaleka, kapena nzeru idzakhala cabe.

9. Pakuti ife tidziwa mderamdera, ndimo tinenera mderamdera.

10. Koma pamene cangwiro cafika, tsono camderamdera cidzakhalacabe.

1 Akorinto 13