1 Akorinto 10:19-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndinena ciani tsono? kuti coperekedwa nsembe kwa mafano ciri kanthu? Kapena kuti fane liri kanthu kodi?

20. Koma nditi kuti zimene amitundu apereka nsembe azipereka kwa ziwanda; ndipo sindifuna kuti inu muyanjane ndi ziwanda.

21. Simungathe kumwera cikho ca Ambuye, ndi cikho ca ziwanda; simungathe kulandirako ku gome la Ambuye, ndi ku gome la ziwanda.

22. Kapena kodi ticititsa nsanje Ambuye? Kodi mphamvu zathu ziposa iye?

23. Zinthu zonse ziloleka; koma sizipindula zonse. Zinthu zonse ziloleka; koma sizimanga zonse.

24. Munthu asafune zace za iye yekha, kama za mnzace.

25. Conse cogulitsidwa pa msika wa nyama, mudye, osafunsa kanthu cifukwa ca cikumbu mtima;

26. pakuti dziko lapansi liri la Ambuye, ndi kudzala kwace.

27. Ngati wina wa osakhulupira akuitanani, ndipo mufuna kupita; mudye comwe ciikidwa kwa inu, osafunsa kanthu, cifukwa ca cikumbu mtima.

1 Akorinto 10