13. Kodi Kristu wagawika? Kodi Paulo anapacikidwa cifukwa ca inu? Kapena kodi munabatizidwa m'dzina la Paulo?
14. Ndiyamika Mulungu kuti sindinabatiza mmodzi yense wa inu, koma Krisipo ndi Gayo;
15. kuti anganene mmodzi kuti mwabatizidwa m'dzina langa.
16. Koma ndinabatizanso a pa banja la Stefana; za ena, sindidziwa ngati ndinabatiza wina yense.
17. Pakuti Kristu sanandituma ine kubatiza, koma kulalikira Uthenga Wabwino, si mu nzeru ya mau, kuti mtanda wa Kristu ungayesedwe wopanda pace.
18. Pakuti mau a mtanda ali ndithu cinthu copusa kwa iwo akutayika, koma kwa ife amene tirikupulumutsidwa ali mphamvu ya Mulungu.
19. Pakuti kulembedwa,Ndidzaononga nzeru za anzeru,Ndi kucenjerakwa ocenjera odidzakutha.